Wachiwiri Oyamba kwa Mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress yemwenso ndi Sipikala wa Nyumba ya Malamuro mdziko muno, Mai Catherine Gotani Hara wapempha mipingo yonse mdziko muno kuti izilimbikitsa umodzi komanso kulorerana, ponena kuti boma limadalira mipingo pa ntchito zake zachitikuko komanso zokweza miyoyo ya anthu.
A Hara amalankhula izi loweruka pa Ogasiti 31, ku Loudon m'boma la Mzimba pomwe anakayimira Pulezidenti Lazarus Chakwera pa mkumano wawukulu wa Sinodi ya Livingstonia yomwe ndi ya mpingo wa CCAP. Mmawu awo, a Gotani Hara anati Sinodi ya Livingstonia ndi bwenzi lenileni la boma mmagawo osiyanasiyana kuphatikizapo a ulimi ndi maphunziro ndipo kuti mchifukwa chake boma la Pulezidenti Chakwera likuonetsetsa kuti pali kulumikizana nthawi zonse pakati pa boma ndi mpingowu. "A Pulezidenti andituma kuti ndikulimbikitseni kuti mupitilire kukhala amodzi pogwira ntchito za uzimu komanso chitukuko popeza iwo akudziwa kuti muli gawo lofunika kwambiri kuti ntchito yawo ikhale yopepuka poyendetsa dziko. Ndipo iwo akuti musatope kuwawunikira pomwe pakufunika kutero chifukwa Inu ndinu mchele wa dziko" Anatero a Mai Gotani Hara mu uthenga wawo ochokera kwa Pulezidenti Chakwera. Iwo anatsindika kuti Pulezidenti Chakwera ndi okonzeka kugawana masomphenya a chitukuko ndi mpingo wa CCAP Sinodi ya Livingstonia komanso mipingo yonse mdziko muno. Koma Wachiwiri Oyamba kwa Mtsogoleri wa MCP yu anatengerapo mwayi kulimbikitsanso ochita ndale mdziko muno kuti nawoso akhale oyanjana, ponena kuti Malawi ndi mmodzi. Pa mwambowu a Mai Catherine Gotani Hara anapereka thandizo la K5 miliyoni kuchokera kwa Mtsogoleri wa dziko lino, K2 miliyoni kuchokera kwa iwo eni, K1 miliyoni kuchokera kwa nduna ya mtengatenga, a Jacob Hara, komanso K250,000 kuchokera kwa nduna yowona za Chitetezo cha mdziko, a Ken Zikhale Ng'oma. ©️ Copyright Power Global Media Limited. Company Limited by Guarantee (SC547426). All Rights Reserved.
0 Comments
|
AuthorKondanani Chilimunthaka ArchivesCategories |